NSANJA YA MLONDA January 2015 | Boma Lopanda Ziphuphu

Anthu padziko lonse amaona kuti ogwila nchito m’madipatimenti a boma amacita ziphuphu kwambili. Kodi n’zothekadi kukhala ndi boma lopanda ziphuphu?

NKHANI YA PACIKUTO

Vuto la Ziphuphu za m’Boma

Vutoli ndi lalikulu kwambili mwina kuposa mmene mukuganizila.

NKHANI YA PACIKUTO

Ufumu wa Mulungu Ndi Boma Lopanda Ziphuphu

Zinthu 6 zimene zimatsimikizila kuti Ufumu wa Mulungu udzakhala wopanda ziphuphu nthawi zonse.

BAIBO IMASINTHA ANTHU

Coonadi ca m’Baibulo cinandithandiza Kupeza mayankho okhutilitsa

Atate ake atamwalila, Mayli Gündel analeka kukhulupilila Mulungu. N’ciani cinamuthandiza kukhala ndi cikhulupililo ceniceni ndi kupeza mtendele wa m’maganizo?

Amuna Muzisangalatsa Akazi Anu

Banja lingazipeza bwino mwakuthupi, koma siliyenda bwino.

Kodi Mudziŵa?

Malinga ndi mmene Baibulo limanenela, kodi liu lakuti “nduna” limatanthauza ciani? N’cifukwa ciani abusa a m’nthawi ya Baibulo anali kulekanitsa nkhosa ndi mbuzi?

Kodi Tiyenela Kupemphela kwa Yesu?

Yesu anayankha funso limeneli.

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kodi anthu analengedwa ndi Mulungu, kapena anasandulika kucokela ku nyama?