Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Amuna Muzisangalatsa Akazi Anu

Amuna Muzisangalatsa Akazi Anu

KODI mwamuna ayenela kusamalila bwanji mkazi wake? Anthu ambili amaganiza kuti nchito yaikulu ya mwamuna ndi kupezela ndalama banja lake basi. Komabe, akazi ambili amene ali ndi cuma cambili amakhalabe ovutika maganizo ndi amantha. Ponena za mwamuna wake, mkazi wina wa ku Spain wochedwa Rosa anakamba kuti mwamuna wake “anali munthu wabwino kwa anthu ena, koma kunyumba anali munthu wankhanza.” Mkazi wina wa ku Nigeria dzina lake Joy anavomeleza kuti, “Ngati sindinagwilizane ndi zimene amuna anga afuna, io amakamba kuti ‘Ufunika kucita zilizonse zimene ndakamba cifukwa ndine mwamuna wako.’”

Kodi mwamuna angakwanilitse bwanji udindo wake mwacikondi? N’ciani cimene mwamuna afunika kucita kuti nyumba yake ikhale malo abwino kapena a “mpumulo” kwa mkazi wake?—Rute 1:9.

ZIMENE BAIBULO LIMANENA ZA ULAMULILO WA MWAMUNA

Ngakhale kuti Mulungu amaona kuti mwamuna ndi mkazi ndi ofanana, Baibulo limakamba kuti aliyense wa io ali ndi udindo wake m’banja. Lemba la Aroma 7:2 limakamba kuti mkazi wokwatiwa amakhala pansi pa “lamulo la mwamuna wake.” Mabungwe ambili amaika munthu wina kukhala woyang’anila zocitika zonse. Mofananamo, Mulungu anaika mwamuna kukhala mutu wa mkazi. (1 Akorinto 11:3) Amuna ayenela kutsogolela zocitika za m’mabanja ao.

Ngati ndinu mwamuna, kodi muyenela kukwanilitsa bwanji udindo wanu umene Mulungu anakupatsani? Baibulo limati: “Pitilizani kukonda akazi anu monga mmene Kristu anakondela mpingo.” (Aefeso 5:25) Zoonadi, ngakhale kuti Yesu Kristu sanakwatilepo, citsanzo cake cingakuthandizeni kukhala mwamuna wabwino. Tiyeni tione mmene mungacitile zimenezi.

YESU NDI CITSANZO CABWINO KWA AMUNA

Yesu anali kuyesa kupeza njila zotonthozela ena ndi kuwathandiza. Yesu analonjeza onse amene anali ovutika ndi olemedwa ndi mavuto ao kuti: “Bwelani kwa ine, . . . ndipo ndidzakutsitsimutsani.” (Mateyu 11:28, 29) Nthawi zambili, iye anali kuthetsa mavuto ao ndiponso kuwathandiza kukhala pa ubwenzi wabwino ndi Yehova. Mpake kuti anthu ambili anali kukonda kukhala pafupi ndi Yesu cifukwa anali kudziŵa kuti adzawatsitsimula.

Mmene amuna angatengele citsanzo ca Yesu. Pezani njila yothandizila mkazi wanu nchito za pakhomo. Akazi ena  amamva monga mmene Rosa anadandaulila kuti: “Ndinali monga wanchito wa amuna anga.” Koma mwamuna wina amene banja lake likuyenda bwino, dzina lake Kweku anati: “Nthawi zonse ndimafunsa mkazi wanga ngati pali nchito imene ndingamuthandize. Cifukwa cakuti ndimamukonda, sindimacita kuyembekeza kuti andipemphe kumuthandiza kugwila nchito za pakhomo.”

Yesu anali woganizila ena ndi wacifundo. Mkazi wina wosauka anavutika ndi matenda oopsa kwa zaka 12. Pamene anamva kuti Yesu ali ndi mphamvu zocilitsa anthu, “mumtima mwake anali kunena kuti: ‘Ndikangogwila malaya ake akunja okhawo, ndicila ndithu.’” Iye sanalakwitse. Mkaziyo anafika pamene panali Yesu ndi kugwila ulusi wopota wa m’mphepete mwa covala cake ndipo nthawi yomweyo anacila. Anthu ena amaona ngati mkaziyu anacita zinthu modzikuza, koma Yesu anaona kuti mkaziyo anali wovutika. *Mokoma mtima, Yesu anamuuza kuti: “Mwanawe, . . . matenda ako aakuluwo atheletu.” Yesu sanali kufuna kucititsa manyazi mkaziyo kapena kum’dzudzula, koma  anazindikila ululu wa matenda ake. Mwakutelo, anasonyeza kuti anali wacifundo.—Maliko 5:25-34.

Mmene amuna angatengele citsanzo ca Yesu. Pamene mkazi wanu wadwala, muonetseni kuti mumam’ganizila ndipo khalani woleza mtima. Muziona zinthu mmene iye amazionela. Izi n’zimene Ricardo anacita. Iye anati; “Ndikadziŵa kuti mkazi wanga angakhumudwe, ndimasamala kakambidwe kanga kuti ndisamukhumudwitse.”

Yesu anali kukambilana ndi ophunzila ake. Yesu anali kukambilana ndi ophunzila ake powaphunzitsa zinthu zambili. Iye anati: “Zonse zimene ndamva kwa Atate wanga ndakudziŵitsani.” (Yohane 15:15) N’zoona kuti Yesu nthawi zina anali kukhala yekha kuti apeze nthawi yosinkhasinkha ndi kupemphela. Koma nthawi zonse anali kuuza ophunzila ake mmene anali kumvelela. Pa usiku wakuti maŵa aphedwa monga cigaŵenga, Yesu moona mtima anauza ophunzila ake kuti anali “kumva cisoni cofa naco” cifukwa ca mavuto amene anali kudzakumana nao. (Mateyu 26:38) Ngakhale kuti zocita zao sizinam’kondweletse, Yesu sanaleke kulankhula ndi mabwenzi ake.—Mateyu 26:40, 41.

Kuganizila citsanzo ca Yesu kumathandiza munthu kukhala mwamuna ndiponso tate wabwino

Mmene amuna angatengele citsanzo ca Yesu. Muziuza mkazi wanu maganizo anu ndi mmene mukumvelela. Mkazi angadandaule kuti mwamuna wake savutika kulankhula pagulu, koma amakhala cete akakhala panyumba. Komabe, onani mmene mkazi wina dzina lake Ana amamvelela mwamuna wake akamuuza maganizo ake. Iye anati, “Ndimaona kuti mwamuna wanga amandikondadi, ndipo ndimazimva kuti ndine woyandikana naye.”

Pewani kukhala cete pofuna kukhaulitsa mkazi wanu. Mkazi wina anati: “Mwamuna wanga atakhumudwa, analeka kundikambitsa kwa masiku angapo. Ndipo ndinadziona kukhala wamlandu ndi wosafunika.” Komabe, mwamuna wina dzina lake Edwin amayetsetsa kutengela citsanzo ca Yesu. Iye anati: “Ndikakwiya, sindimacitapo kanthu nthawi imeneyo. Ndimayembekezela nthawi yabwino yakuti tikambilane za vutolo ndi kuona mmene tingalithetsele.”

Joy, amene tachula kuciyambi kwa nkhani ino, waona kuti mwamuna wake wasintha kucokela pamene anayamba kuphunzila Baibulo ndi Mboni za Yehova. Joy anati: “Iye wasintha ndipo amayesetsa kukhala mwamuna wacikondi potengela citsanzo ca Yesu.” Mabanja ambili akupindula cifukwa cotsatila malangizo a m’Baibulo. Kodi inunso mufuna kupindula ndi malangizo a m’Baibulo amenewo? Ngati n’conco, pemphani wa Mboni za Yehova kuti muziphunzila naye Baibulo kwaulele..

^ par. 10 Malinga ndi Cilamulo ca Mose, matenda a mkazi ameneyo anam’cititsa kukhala wodetsedwa, ndipo aliyense womukhudza anali kuonedwa kukhala wodetsedwa.—Levitiko 15:19, 25.