Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kuyankha Mafunso a m’Baibulo

Kodi n’zotheka kukhala m’dziko lopanda umphawi?

Kodi Mulungu adzathetsa bwanji umphawi padzikoli?—Mateyu 6:9, 10.

Anthu mamiliyoni amafa caka ciliconse cifukwa ca matenda obwela kaamba ka kucepelekela kwa cakudya. Ngakhale kuti maiko ambili ndi olemela, anthu oculuka ali mu umphawi wadzaoneni. Baibulo limatiuza kuti umphawi wavutitsa anthu kwa nthawi yaitali.—Ŵelengani Yohane 12:8.

Kuti umphawi uthe, pafunika boma lamphamvu la padziko lonse limene lingagaŵe cuma ca dziko mosakondela. Boma limenelo lidzafunika kuthetsa nkhondo cifukwa ndilo vuto lalikulu limene limacititsa umphawi. Mulungu walonjeza boma la padziko lonse limene lidzathetsa mavuto onse.—Ŵelengani Daniel 2:44.

Ndani angathetse umphawi?

Mulungu wasankha Mwana wake, Yesu, kuti adzalamulile anthu onse. (Salimo 2:4-8) Yesu adzapulumutsa anthu osauka ndipo adzathetsa kupondelezana komanso ciwawa.—Ŵelengani Salimo 72:8, 12-14.

Yesu, monga “Kalonga Wamtendele,” adzakhazikitsa mtendele ndi citetezo padziko lonse lapansi. Anthu onse padziko lapansi adzakhala ndi nyumba zaozao, adzasangalala kugwila nchito yokhutilitsa, ndipo adzakhala ndi cakudya coculuka.—Ŵelengani Yesaya 9:6, 7; 65:21-23.