Kodi Pali Wina Amene Akumvetsela?
Anthu ena amaganiza kuti kupemphela n’kutaya nthawi ndipo palibe amene amamvetsela. Anthu ena amapemphela, koma amaona kuti sayankhidwa. Munthu wina amene sakhulupilila kuti kuli Mulungu anaganiza mmene Mulungu alili ndipo anapemphela kuti: “Ngati muliko, mundiŵeleŵeseko cabe.” Koma iye anati Mulungu “anangokhala cete.”
Komabe, Baibulo limatitsimikizila kuti Mulungu amamva mapemphelo. Ameneyo ndi Mulungu, wamkulu koposa m’cilengedwe conse. Baibulo limakamba za anthu akale kuti: “Mosakayikila, iye [Mulungu] adzakukomela mtima akadzamva kulila kwako. Akadzangomva kulila kwakoko, iye adzakuyankha.” (Yesaya 30:19) Baibulo limakambanso kuti: “Koma pemphelo la anthu oongoka mtima limam’sangalatsa.”—Miyambo 15:8.
Yesu anapemphela kwa Atate wake “ndipo anamumvela.”—Aheberi 5:7
Baibulo limatiuzanso zitsanzo za anthu amene mapemphelo ao anayankhidwa. Limanena kuti Yesu anapeleka “mapemphelo opembedzela. . . kwa amene anali wokhoza kumupulumutsa” ndipo “anamumvela.” (Aheberi 5:7) Zitsanzo zina timazipeza pa Danieli 9:21 ndi 2 Mbiri 7:1.
Nanga, n’cifukwa ciani anthu ena amaona kuti mapemphelo ao sayankhidwa? Kuti mapemphelo athu aziyankhidwa, tiyenela kupemphela kwa Mulungu wochulidwa m’Baibulo, Yehova, * osati kwa mulungu wina kapena kwa makolo amene anamwalila kalekale. Mulungu amafuna kuti ‘tizipempha mogwilizana ndi cifunilo cake’ zinthu zimene amavomeleza. Ngati tipempha mwa njila imeneyi, Mulungu “amatimvela.” (1 Yohane 5:14) Conco, kuti mapemphelo athu aziyankhidwa, tifunika kudziŵa Mulungu wochulidwa m’Baibulo ndi cifunilo cake.
Anthu ambili amakhulupilila kuti pemphelo sicinthu congocita mwamwambo cabe, koma Mulungu amamvetsela mapemphelo ndipo amayankha. Munthu wina dzina lake Isaac wa ku Kenya anati: “Ndinapemphela kuti ndimvetsetse Baibulo. Posapita nthawi, munthu wina anabwela ndi kundithandiza kumvetsetsa Baibulo.” Nayenso Hilda wa ku Philippines, anafuna kuleka kukoka fodya. Anayesa mobwelezabweleza koma analephela. Mwamuna wake anamuuza kuti: “Pemphela kwa Mulungu kuti akuthandize.” Iye anacita zimene mwamuna wake anakamba ndipo anati: “Ndinadabwa mmene Mulungu anandithandizila. Ndinayamba kuleka pang’onopang’ono kukoka fodya, mpaka ndinalekelatu.”
Kodi Mulungu angakuthandizeni pa mavuto anu mukam’pempha mogwilizana ndi cifunilo cake?
^ par. 5 Baibulo limati dzina la Mulungu ndi Yehova.