Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

NKHANI YA PACIKUTO MUNGACITE CIANI KUTI MUPINDULE NA ZIMENE MUŴELENGA M’BAIBO?

Mungacite Ciani Kuti Kuŵelenga Baibo Kuzikukondweletsani?

Mungacite Ciani Kuti Kuŵelenga Baibo Kuzikukondweletsani?

Kodi mumakondwela pamene muŵelenga Baibo kapena simukondwela? Kuti muzikondwela, zimadalila mmene mumaiŵelengela. Onani zimene mungacite kuti muzikonda kuŵelenga Baibo ndi kuti muzikondwela pamene muŵelenga.

Sankhani Baibo yodalilika ndi ya mau osavuta kumva. Ngati muŵelenga Baibo imene ili na mau ambili ovuta kumva, acikale, kapena amene simuwadziŵa, simungakondwele poiŵelenga. Conco, sankhani Baibo imene muli mau osavuta kumva amene angakufikeni pamtima. Komanso iyenela kukhala yomasulidwa molongosoka. *

Muziseŵenzetsa zipangizo zamakono. Masiku ano, Baibo siipezeka cabe monga buku lopulintiwa, koma imapezekanso pa kompyuta. Mabaibo ena mukhoza kuwaŵelengela pa intaneti kapena mungacite daunilodi kuti muziwaŵelengela pa kompyuta, pa tabuleti, kapena pa foni yanu. Mabaibo ena ali na zinthu zimene zingakuthandizeni kuyelekezela mavesi amene muŵelenga ndi mavesi ena a m’Baibo, kapena kuyelekezela mmene Mabaibo ena anamasulila mavesiwo. Ngati simufuna kucita kuŵelenga Baibo, mungamvetsele mau a m’Baibo ojambulidwa. Anthu ambili amakonda kumvetsela nyimbo ndi zinthu zina poyenda, powacha, kapena pocita zinthu zina. Kodi inu mungayeseko kumvetsela Baibo pocita zina mwa zinthu tachulazi?

Muziseŵenzetsa zida zothandiza pophunzila Baibo. Zida zothandiza pophunzila Baibo zingakuthandizeni kumvetsetsa zimene muŵelenga. Pali mamapu oonetsa malo a m’Baibo amene angakuthandizeni kudziŵa malo ochulidwa m’Baibo ndi kumvetsetsa nkhani zimene muŵelenga. Komanso nkhani za m’magazini ino kapena zopezeka pa webusaiti ya jw.org, pa cigawo cakuti “Zimene Baibulo Limaphunzitsa,” zingakuthandizeni kumvetsetsa tanthauzo la malemba ambili.

Muzisintha-sintha kaŵelengedwe kanu. Ngati muona kuti kuŵelenga Baibo kucokela kuciyambi mpaka kumapeto n’kocititsa ulesi, mungayambile kuŵelenga nkhani zimene zimakukondweletsani ngako. Ngati mufuna kudziŵa bwino anthu ochulidwa m’Baibo, mungayese kuiphunzila motsatila maina a anthu a m’Baibo. Njila imeneyi yaonetsedwa m’bokosi yakuti “ Phunzilani za Anthu Ochulidwa m’Baibo Kuti Muimvetsetse.” Komanso ngati mufuna, mungaŵelenge Baibo motsatila mitu ya nkhani kapena motsatila ndondomeko ya mmene zinthu zinacitikila. Kodi mungayeseko kucita zimenezi?

^ par. 4 Anthu ambili aona kuti Baibulo la Dziko Latsopano la Malemba Opatulika ni lolongosoka, lodalilika, ndi losavuta kumva. Baibo imeneyi ni yomasulidwa na Mboni za Yehova, ndipo ipezeka m’zitundu zoposa 130. Mungacite daunilodi Baibo imeneyi pa webusaiti ya jw.org kapena mungacite daunilodi JW Library. Ndipo ngati mufuna, mungapemphe a Mboni za Yehova kuti akubweletseleni Baibo kunyumba kwanu.