NYIMBO 130
Khalani Wokhululuka
(Salimo 86:5)
-
1. Atate Yehova,
Anapeleka Yesu
Kuti iye atifele,
Acotsepo na imfa.
Tikasintha na kulapa,
Tikasiya zoipa,
Mu dzina la Yesu Khristu
Tidzakhululukidwa.
-
2. Monga ‘tate wathu,
Tikhale na cifundo;
Tikhululukile ena;
Tionetse cikondi.
Ticitilane ulemu,
Ndipo tipililane.
Ngati tikhululukila
Tidzakhululukidwa.
-
3. Tonse tionetse
Mkhalidwe wa cifundo.
Tisadane na abale,
Tiŵakomele mtima.
Tikatengela Yehova
Wopambana m’cikondi,
Tidzakhululukiladi
Monga Atate wathu.
(Onaninso Mat. 6:12; Aef. 4:32; Akol. 3:13.)