NYIMBO 98
Malemba ni Ouzilidwa na Mulungu
(2 Timoteyo 3:16, 17)
-
1. Mu dziko ili la mdima,
Timaona kuwala,
Kwa Mau a M’lungu wathu,
Opezeka mu Baibo.
-
2. Yehova anatipatsa
Mau ouzilidwa.
Kuti atitsogolele
Mu njila ya cilungamo.
-
3. Mau a Yehova M’lungu
Amatilimbikitsa.
Iye ni Atate wathu,
Tidziŵa amatikonda.
(Onaninso Sal. 119:105; Miy. 4:13.)