Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Sitidzakuiŵalani

Sitidzakuiŵalani

Daunilodi:

  1. 1. Ngati mvula na cimphempo

    Zaononga nyumba na zinthu zanu,

    M’sakaikile, simuli mwekha.

    Tili namwe.

    Yehova adzakuthandizani.

    (KOLASI)

    Sitizayetsa kukuiŵalani

    Pakagwa vuto sitidzalephela

    Kuthandiza kuti imwe

    Mulimbedi mtima

    Tithandizadi, ndise banja lanu.

  2. 2. Pa mavuto tili namwe

    Na cikondi cowala ngati dzuŵa.

    Conde dziŵani tikukondani

    Cikondici cipangitsa tikuthandizeni.

    (KOLASI)

    Sitidzayesa kukuiŵalani

    Pakagwa vuto sitidzalephela

    Kuthandiza kuti imwe

    Mulimbedi mtima

    Tithandidzadi, ise ndise banja lanu.

    Tithandidzadi, ndise banja lanu.