Onani zimene zilipo

Onani nkhani zake

Tizikhululukilana

Tizikhululukilana

Daunilodi:

  1. 1. Munali kufuna zabwino

    Mumanicitilanso cifundo

    Koma munasokoneza mawu

    Moti misozi ikugwa

    Sitinamvetsetsane

    (KOLASI)

    Dzuŵali lisanangene

    Nabwela tikambitsilane

    Tikhululukilane tisazondane

    Tikhalebe mwamtendele

  2. 2. Kugwilizana nikovutadi

    Mawu olatsa mtima aŵaŵa

    Koma kukhululukilana

    Ndiye kungatithandize

    Kukhala na mtendele

    (KOLASI)

    Dzuŵali lisanangene

    Nabwela tikambitsilane

    Tikhululukilane tisazondane

    Tikhalebe mwamtendele

    (BILIJI)

    Palibe cimene cingalekanitse

    Ubale wathu

    Iŵalako, khululukadi

    Tizalimbitsa ubwenzi

    (KOLASI)

    Dzuŵali lisanangene

    Nabwela tikambitsilane

    Tikhululukilane tisazondane

    Tikhalebe mwamtendele

    Mwacikondi, tikhululukilane