Onani zimene zilipo

Kodi Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society N’ciani?

Kodi Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society N’ciani?

 Bungwe la Watch Tower Bible and Tract Society of Pennsylvania linakhazikitsidwa mu 1884 motsatila malamulo a ku Pennsylvania m’dziko la America, ndipo colinga cake si kupeza ndalama ayi. Mboni za Yehova zimaseŵenzetsa bungweli pocita zinthu monga kufalitsa Mabaibo na mabuku ena ofotokoza Baibo.

 Zolinga za bungweli n’zokhudza “cipembedzo, maphunzilo ndiponso kuthandiza anthu.” Koma colinga cake cacikulu ni “kulalikila na kuphunzitsa uthenga wa Ufumu wa Mulungu umene Mfumu yake ni Yesu Khristu.” Kuti munthu akhale m’bungweli amacita kupemphedwa, ndipo sizidalila kuculuka kwa ndalama zimene iye amacita copeleka. Anthu amene ali m’bungweli amathandiza Bungwe Lolamulila la Mboni za Yehova.

Mabungwe Enanso

 Kuwonjezela pa bungweli, a Mboni za Yehova amaseŵenzetsanso mabungwe ena m’mayiko osiyana-siyana. Ena mwa mabungwe amenewa ni akuti, “Watch Tower” kapena “Watchtower.”

 Mabungwewa akhala akuthandiza Mboni za Yehova pa nchito zotsatilazi:

  •   Kulemba na kufalitsa mabuku. Tafalitsa Mabaibo pafupi-fupi 220 miliyoni ndiponso mabuku ena pafupi-fupi 40 biliyoni m’vitundu voposa 900. Pa webusaiti yathu ya jw.org munthu akhoza kuŵelenga Baibo m’vitundu voposa 160 popanda kulipila. Akhozanso kupeza mayankho a mafunso monga “Kodi Ufumu wa Mulungu N’ciani?

  •   Maphunzilo. Timakhala na masukulu osiyana-siyana ophunzitsa Baibo. Mwacitsanzo, kuyambila mu 1943, a Mboni za Yehova oposa 9,000 atsiliza maphunzilo a Sukulu ya Giliyadi Yophunzitsa Baibo, ndipo atumizidwa kukatumikila monga amishonale kapena kukathandiza pa nchito yolalikila kumaiko ena. Wiki iliyonse, anthu mamiliyoni kuphatikizapo amene si Mboni, amaphunzitsidwanso pamisonkhano yathu ya mpingo. Timakhalanso na masukulu ophunzitsa anthu kuŵelenga na kulemba, ndipo buku limene timaseŵenzetsa pa sukuluyi lafalitsidwa m’vitundu 120.

  •   Kuthandiza anthu. Timapeleka cithandizo kwa anthu amene akumana na mavuto. Mwacitsanzo, tinathandiza anthu pa nthawi ya nkhondo imene inacitika ku Rwanda mu 1994 komanso pa nthawi ya civomezi cimene cinacitika ku Haiti mu 2010.

 Ngakhale kuti timacita zinthu zambili poseŵenzetsa mabungwewa, nchito yathu yolalikila sidalila pa mabungwe amenewa. Mkhristu aliyense ali na udindo wotsatila lamulo limene Mulungu anapeleka lakuti tizilalikila na kuphunzitsa uthenga wabwino. (Mateyu 24:14; 28:19, 20) Timakhulupilila kuti Mulungu amatithandiza pa nchito yathu imeneyi, ndipo adzapitilizabe ‘kuikulitsa.’—1 Akorinto 3:6, 7.